Koma lipoti la hotela ya amaryllis lidzatuluka?

Chikaiko chayambanso kukula ngati lipoti la kafukufuku wa momwe hotela ya Amaryllis idagulitsidwira libwere mu Nyumba ya Malamulo pa mkumano wa aphungu womwe uli mkatiwu kaamba ka zomwe adindo osiyanasiyana ku nyumbayo akunena. Sabata zitatu zapitazo, wapampando wa komiti yoona momwe chuma cha boma chimayendera (PAC) yomwe ikufufuza nkhaniyo a Steve Malondera adatsimikiza kuti lipotilo … The post Koma lipoti la hotela ya amaryllis lidzatuluka? appeared first on Nation Online.

Koma lipoti la hotela ya amaryllis lidzatuluka?

Chikaiko chayambanso kukula ngati lipoti la kafukufuku wa momwe hotela ya Amaryllis idagulitsidwira libwere mu Nyumba ya Malamulo pa mkumano wa aphungu womwe uli mkatiwu kaamba ka zomwe adindo osiyanasiyana ku nyumbayo akunena.

Sabata zitatu zapitazo, wapampando wa komiti yoona momwe chuma cha boma chimayendera (PAC) yomwe ikufufuza nkhaniyo a Steve Malondera adatsimikiza kuti lipotilo ndilakupsa ndipo liperekedwa pa mkumano wa aphungu womwe ulimkatiwu.

Sanakapereke umboni: a Zamba.| Nation

 Koma Lolemba lapitali, mtsogoleri wa Nyumba ya Malamulo a Jappie Mhango adauza nyuzipepala ya The Nation ya Lachiwiri kuti sakukhulupilira zoti lipotilo ndilakupsa kaamba koti mboni yaikulu yomwe ndi amene adali mlembi wamkulu wakale waboma a Colleen Zamba sadalankhulepo.

 “Sindidalandile chitsimikizo chili chonse choti lipoti limenero lidapsa ndipo ndikukaika ngati lidapsadi chifukwa mpakana pano, sindidamve kuti a Zamba omwe ndi mboni yofunikira kwambiri pankhaniyi adapelekera umboni wawo,” adatero a Mhango.

 Koma mkatikati mwa kafukufuku, a Zamba adauza komitiyo kuti sangathe kudzaperekera umboni wawo pa nkhaniyo kaamba koti akulandira thandizo la zaumoyo kunja kwa dziko lino komanso akuyankha zokhudza nkhani yomweyi mkhothi.

Chodabwitsanso kwambiri n’chakuti mkumano utayamba Lachiwiri, Sipikala wa Nyumba ya Malamulo a Sameer Suleman adauza komitiyo kuti ipange changu kuphika lipotilo ndipo liwapeze ku ofesi yawo kuti idzalowe mu Nyumba ya Malamulo.

Ndondomeko yopelekera malipoti amakomiti a Nyumba ya Malamulo imati, komiti ikamaliza kuphika lipoti lake, imayenera kukalipeleka ku ofesi ya a sipikala isadapite ku Nyumba ya Malamulo kuti aphungu akalikambirane.

Pa mkumano wapitawo, a Malondera adauzanso Nyumba ya Malamulo kuti PAC idamaliza kafukufuku ndipo lipoti lidapsa, koma nyumbayo kudzera mwa mtsogoleri wake a Mhango idabweza lipotilo kuti lidzabwere pokhapokha a Zamba akadzaperekera umboni wawo.

 Koma Amalawi ena ati lipotilo likufunika kuti anthu, makamaka eni ndalama zomwe zidagwiritsidwa ntchito pankhani yonseyo (opuma pantchito), adziwe chomwe chidachitika ndi anthu omwe ali pambuyo pa zimenezi.

 A Jaquerine Kulamkono aku Sector 7 ku Area 25 ku Lilongwe adati Nyumba ya Malamulo ili ndi udindo wopereka malipoti a zomwe zikuchitika kaamba koti anthu adawapatsa mphamvu kudzera mu voti kuti azikafukula zinthu n’kumapereka malipoti osati kubisa.

 “Tsopano anthu ayamba kukaikira kuti mwina pali chomwe chikubisidwa.  Nanga monse muja tizingokhalira kudikilira lipoti limodzimodzilo? Pamwamba pa nkhani zina zofunikira kwambiri, pa mkumano umenewu, atipatse lipoti la Amaryllis,” adatero a Kulamkono.

The post Koma lipoti la hotela ya amaryllis lidzatuluka? appeared first on Nation Online.