‘Mitengo yomangira ma CDSS yanyanya’
Nduna yoona za maphunziro a Bright Msaka achenjeza kuti ndalama zonse za m’thumba la chitukuko la Constituency Development Fund (CDF) zikhonza kutha pongomangira sukulu za m’madera za CDSS ngati eni kampani sasintha mchitidwe woonjezera udyo mitengo yawo yomangira sukuluzo. A Msaka adanena izi Lachiwiri m’Nyumba ya Malamulo poyankha funso la phungu wa dera lapakati ku … The post ‘Mitengo yomangira ma CDSS yanyanya’ appeared first on Nation Online.
Nduna yoona za maphunziro a Bright Msaka achenjeza kuti ndalama zonse za m’thumba la chitukuko la Constituency Development Fund (CDF) zikhonza kutha pongomangira sukulu za m’madera za CDSS ngati eni kampani sasintha mchitidwe woonjezera udyo mitengo yawo yomangira sukuluzo.
A Msaka adanena izi Lachiwiri m’Nyumba ya Malamulo poyankha funso la phungu wa dera lapakati ku Nsanje, a Francis Kasaila, pa chifukwa chomwe mtengo womangira sukulu za boma ukuposa K1 biliyoni sukulu imodzi pamene bungwe lina la ku Germany lidakwanitsa kumanga sukulu ina m’boma la Mwanza pa mtengo wa 110 000 Euro zomwe ndi pafupifupi K250 miliyoni.

Msaka adatsimikiza kuti boma lidalandiradi ngati mphatso sukulu ya tunthu yokhala ndi nyumba 6 za aphunzitsi kuchokera ku bungwe la Green Helmets m’dera la kuzambwe m’boma la Mwanza yomwe idamangidwa ndi ndalama zochepazo.
Ndunayi idati ndalama zomwe kampani za Chimalawi zikumatchula kuti zigwirire ntchito yomanga ma CDSS zikumaika ngakhale K4 biliyoni; mtengo omwe ukhonza kuchititsa kuti dziko lino liyambe kukanika kumanga sukulu za sekondale chifukwa ndalama zonse za CDF zokwana K5 biliyoni zizithera pa sukulu imodzi yokha.
“Chachidziwikire n’choti amene adamanga sukulu tikuitchulayi sadaphatikize phindu lomwe adindo ena amafuna kupeza mwachinyengo, komanso kuti ntchito zina monga kupereka mchenga adagwira ndi anthu a m’mudzi.
“Komabe ngakhale mutaphatikiza phindu ndi ndalama zolipirira ntchito zomwe anthu a m’mudzi anachita, mitengo yomwe tikumva ya K1 biliyoni kaya K4 biliyoni pomanga CDSS yanyanya zedi ndipo ndi yosavomerezeka,” adatero a Msaka.
Ndipo adati undunawo ugwira ntchito limodzi ndi Nyumba ya Malamulo ndi magulu ena onse okhudzidwa kuonetsetsa kuti ntchito yomanga sukulu isakhale njira yobera ndalama za nzika za Malawi.
Poyambirira, a Kasaila adati mpofunika kuti Nduna ya Maphunziro ifotokozere ku Nyumba ya Malamulo mmene bungwe la ku Germany limeneli lidakwanitsira kumanga sukulu ndi ndalama zochepa kuti aphungu aphunzirepo ndi kugwiritsa ntchito bwino ndalama za CDF pomanga sukulu zotere m’madera mwawo.
“Mwina ndi ndalama zokwana K3.6 biliyoni zomwe zaperekedwa pano kuti tigwirire ntchito zomangamanga, tikhoza kumanga nyumba zochuluka osati kumanga nyumba ya zipinda ziwiri zophunziliramo pa mtengo wa K200 miliyoni yomwe njoposa ndalama zonse zomwe abwenzi a ku Germany ndi anthu a m’mudziwa adagwiritsa ntchito pomanga nyumba zonsezi ku Mwanza” adatero a Kasaila.
Iwo adayamikiranso nyumba zomwe zidamangidwa ku Mwanza kuti zidali zooneka za pa mwamba poyerekeza ndi ndalama zochepa zomwe zidalowa pa ntchitoyo osati mmene zimakhalira ndi zomangidwa pa mitengo yopitirira K1 biliyoni.
“Zithunzi zomwe taona zikusonyeza kuti nyumba za aphunzitsi, zochitiramo maphunziro a zasayansi, makalasi, ngakhalenso malo ena ndi zabwino kwambiri chonsecho zonse anazimanga pamtengo wa 110 000 euro basi,” adatero Kasaila.
Aphungu osiyanasiyana, kuphatikizapo Wachiwiri Woyamba wa Sipikala wa Nyumba ya Malamulo, Victor Musowa, anagwirizana kuti nkhaniyi ndi yofunika kwambiri ponena kuti ndalama za misonkho ya Amalawi n’zofunika kuziteteza kuti zisamagwiritsidwe ntchito molakwika.
The post ‘Mitengo yomangira ma CDSS yanyanya’ appeared first on Nation Online.
